Top Songs By Sir Paul Banda
Similar Songs
Credits
PERFORMING ARTISTS
Sir Paul Banda
Vocals
COMPOSITION & LYRICS
Sir Paul Banda
Composer
PRODUCTION & ENGINEERING
Sir Paul Banda
Producer
Lyrics
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Tingalilire zambirimbiri tiiwala chimodzi
Moyowu ngosowa
Anthu mzeru zingachuluke kupanga zambiri
Sadzapanga moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Anthufe padziko pano timalilira zambiri
Chopambana ndi moyo
Ngakhale inu mumuukire kuti saakukondani
Muganizire moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Abwenzi athu ambirimbiri anatisiya
Anawalanda moyo
Angakhale ndingasauke ndidzathokoza chauta
Pondisungira moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Anthu ena anafunitsitsa akanakhala moyo
Koma analephera
Tinthokoze Chauta poti mpaka leroli
Tilinawo moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Mdzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Ndikuyamika Ambuye ine
Wondisungira moyo
Ndidzatamanda Ambuye ine
Wondipatsa moyo
Written by: Paul Banda